Monday, September 16, 2019

Fanizo Lozama

Fanizo lakuya ili. Mwini chuma anatenga ndalama zisanu napatsa wantchito oyamba, ndalama ziwiri kwa wanchito wina, komanso ndalama imodzi kwa wantchito omaliza. Ndipo malemba anenetsa kuti, aliyense anapatsidwa malinga ndi luntha lake.

Mwini chuma anapita ulendo wake kwa nthawi ndithu. Uja analandira zisanu analowa pa msika, nachita malonda ndi kupeza phindu la ndalama zina zisanu. Chimodzimodzi uja analandira ndalama ziwiri, nayenso analowa pa msika, natakata ndi kupeza phindu la ndalama zina ziwiri.

Koma uja analandira ndalama imodzi uja, aaaa za chisoni, anakumana ndi achina Chakwera, Chilima ndi mnyamata wawo Mtambo, a nthawi imeneyo. Ali “amwene, bwana wanu uja ndi wankhanza. Taonani chuma cha dziko sichikuyenda bwino, musalowe pa msika amwene, mubetsa ndalama yonseyo. Ndiponso onani ulamuliro wa Kaesala, wa nkhanza. Iwe ndi muyuda, ungapange phindu mu ufumu wa Aroma? Udikire ife tikatenga boma. Udzakweta.”

Ndiye yalani bodza pamene paja. “Waona, ma demo tikupangawa, tigwetsa boma. Titenga boma limeneli.”

Ndiye kunali ana osowa chochita, achina Kunkuyu a nthawi imeneyo, kumayenda mmidzi ya Ayuda, amvekere, “tiyeni ku mademo, tikufuna tilamule dzikoli ife tikupatseni zosowa zanu.”

Basi, uja olandira ndalama imodzi kupusisika, eti kukwilira ndalama ija, mu dothi.

Patapita nthawi, mwini chuma balamanthu, wafika. Uja analandira ndalama zisanu anabweretsa ndalama khumi, atapanga phindu. Chimodzimodzi wa ndalama ziwiri uja, anapeza phindu la ndalama zina ziwiri. Kwa awiriwa mwini chuma anati, “akapolo okhulupirka inu, lowani mu chokondwelero cha atate anga, ndipo mudzapatsidwa zochuluka.”

Naye uja wa ndalama imodzi anafika, amvekele: “Mbuye wanga, ndinadziwa kuti ndinu munthu wa nkhanza, okolola pomwe simunafese, ndi kututa pomwe simunazale. Ine ndinaopa mtima wanu wa nkhanzawo ndipo ndalama yanu ndinaikwilira mu nthaka. Nayi, kwayani ndalama yanu.”

Chosadziwa. Mwini chuma anati, “Kapolo osakhulupirika iwe. Ngati unadziwa kuti ndine wankhanza, okolora pomwe sindinafese, bwanji sunatenge ndalama yanga kukaisunga ku banki kuti ipange chiongoladzanja? Mulandeni ndalamayo, ndipo muipeleke kwa uyo ali ndi khumi. Pakuti kwa iye ali nazo zochuluka, yemweyo adzapatsidwa.”

Achina Chakwera, Chilima ndi mnyamata wao Mtambo osaoneka. Mwana osowa chochita Kunkuyu kuli ziiii. Atamupweteketsa munthu. Wa ntchito uyu anasauka, chifukwa chomvera anthu a nkhanza kwa amphawi. Antchito ena awiri aja amatakata, kumadya pa ndalama pomwepo, kwinaku akupanga phindu. Uyu amamvera bodzayu, kukwilira ndalama yake, kumasowanso chakudya. Banja lake kumavutika. Ati kudikira nthawi imene a mademo adzatenge boma.

Haaaaaaa! Kupusa.

No comments: